Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 144

1Atamandike Yehova Thanthwe langa, amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; zala zanga kumenya nkhondo.

2Iye ndiye Mulungu wanga wachikondi ndi malo anga otetezedwa, linga langa ndi mpulumutsi wanga, chishango changa mmene ine ndimathawiramo, amene amagonjetsa mitundu ya anthu pansi panga.

3Inu Yehova, munthu nʼchiyani kuti mumamusamalira, mwana wa munthu kuti muzimuganizira?

4Munthu ali ngati mpweya; masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.

5Ngʼambani mayiko akumwamba, Inu Yehova, ndipo tsikani pansi; khudzani mapiri kuti atulutse utsi.

6Tumizani zingʼaningʼani ndi kubalalitsa adani; ponyani mivi yanu ndi kuwathamangitsa.

7Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba; landitseni ndi kundipulumutsa, ku madzi amphamvu, mʼmanja mwa anthu achilendo,

8amene pakamwa pawo ndi podzala ndi mabodza, amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

9Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu; ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,

10kwa Iye amene amapambanitsa mafumu, amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.

11Landitseni ndi kundipulumutsa, mʼmanja mwa anthu achilendo, amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza, amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

12Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino, ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.

13Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza ndi zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda pa mabusa athu.

14Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera. Sipadzakhala mingʼalu pa makoma, sipadzakhalanso kupita ku ukapolo, mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.

15Odala anthu amene adzalandira madalitso awa; odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath