Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 141

1Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine. Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.

2Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.

3Yehova ikani mlonda pakamwa panga; londerani khomo la pa milomo yanga.

4Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa; kuchita ntchito zonyansa pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa; musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.

5Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo; andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga. Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.

6Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri, ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino.

7Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza, ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.”

8Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse; ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa.

9Mundipulumutse ku misampha imene anditchera, ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera.

10Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo, mpaka ine nditadutsa mwamtendere.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath