MASALIMO 140
1Landitseni Yehova kwa anthu oyipa; tetezeni kwa anthu ankhanza,
2amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.
3Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka; pa milomo yawo pali ululu wa mamba. Sela
4Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa; tchinjirizeni kwa anthu ankhanza amene amakonza zokola mapazi anga.
5Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika; iwo atchera zingwe za maukonde awo ndipo anditchera misampha pa njira yanga. Sela
6Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.” Imvani kupempha kwanga Yehova.
7Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu, mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.
8Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova; musalole kuti zokonza zawo zitheke, mwina iwo adzayamba kunyada. Sela
9Mitu ya amene andizungulira iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.
10Makala amoto agwere pa iwo; aponyedwe pa moto, mʼmaenje amatope, asatulukemonso.
11Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko; choyipa chilondole anthu ankhanza.
12Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.
13Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu, ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath