MASALIMO 138
1Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
2Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse.
3Pamene ndinayitana, munandiyankha; munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
4Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova, pamene amva mawu a pakamwa panu.
5Iwo ayimbe za njira za Yehova, pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
6Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa, koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
7Ngakhale ndiyende pakati pa masautso, mumasunga moyo wanga; mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga, mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
8Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine; chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha musasiye ntchito ya manja anu.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath