MASALIMO 137
1Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira pamene tinakumbukira Ziyoni.
2Kumeneko, pa mitengo ya misondozi tinapachika apangwe athu,
3pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo. Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo; iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”
4Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova mʼdziko lachilendo?
5Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu, dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.
6Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu, ngati sindiyesa iwe chimwemwe changa chachikulu.
7Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita pa tsiku limene Yerusalemu anagonja. Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi mpaka pa maziko ake!”
8Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa, wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera pa zimene watichitira.
9Amene adzagwira makanda ako ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath