MASALIMO 132
1Inu Yehova, kumbukirani Davide ndi mavuto onse anapirira.
2Iye analumbira kwa Yehova ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
3“Sindidzalowa mʼnyumba mwanga kapena kugona pa bedi langa:
4sindidzalola kuti maso anga agone, kapena zikope zanga ziwodzere,
5mpaka nditamupezera malo Yehova, malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”
6Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata, tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
7“Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo; tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
8‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira, Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
9Ansembe anu avekedwe chilungamo; anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’ ”
10Chifukwa cha Davide mtumiki wanu, musakane wodzozedwa wanu.
11Yehova analumbira kwa Davide, lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha: “Mmodzi wa ana ako ndidzamuyika pa mpando waufumu;
12ngati ana ako azisunga pangano langa ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa, pamenepo ana awo adzakhala pa mpando wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”
13Pakuti Yehova wasankha Ziyoni, Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
14“Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi; ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
15Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri; anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
16Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso, ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.
17“Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
18Ndidzaveka adani ake manyazi, koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath