MASALIMO 127
1Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe. Yehova akapanda kulondera mzinda, mlonda akanangolondera pachabe.
2Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa ndi kusagona msanga madzulo, kuvutikira chakudya choti mudye, pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
3Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
4Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja mwa munthu wankhondo.
5Wodala munthu amene motengera mivi mwake mwadzaza. Iwo sadzachititsidwa manyazi pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath