Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 126

1Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati amene akulota.

2Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka; malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe. Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti, “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”

3Yehova watichitira zinthu zazikulu, ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

4Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova, monga mitsinje ya ku Negevi.

5Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.

6Iye amene amayendayenda nalira, atanyamula mbewu yokafesa, adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe, atanyamula mitolo yake.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath