Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 125

1Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.

2Monga mapiri azungulira Yerusalemu, momwemonso Yehova azungulira anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.

3Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama, kuti anthu olungamawo angachite nawonso zoyipa.

4Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino, amene ndi olungama mtima

5Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa. Mtendere ukhale pa Israeli.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath