MASALIMO 11
1Mwa Yehova ine ndimathawiramo. Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti, “Thawira ku phiri lako ngati mbalame.
2Pakuti taona oyipa akunga mauta awo; ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta, pobisala pawo kuti alase olungama mtima.
3Tsono ngati maziko awonongeka, olungama angachite chiyani?”
4Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa.
5Yehova amayesa olungama, koma moyo wake umadana ndi oyipa, amene amakonda zachiwawa.
6Iye adzakhuthulira pa oyipa makala amoto ndi sulufule woyaka; mphepo yotentha idzakhala yowayenera.
7Pakuti Yehova ndi wolungama, Iye amakonda chilungamo; ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath