Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 110

1Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.”

2Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni; udzalamulira pakati pa adani ako.

3Ankhondo ako adzakhala odzipereka pa tsiku lako la nkhondo. Atavala chiyero chaulemerero, kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha, udzalandira mame a unyamata wako.

4Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake: “Ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”

5Ambuye ali kudzanja lako lamanja; Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.

6Adzaweruza anthu a mitundu ina, adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.

7Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira; choncho adzaweramutsa mutu wake.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath