Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 108

1Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu; ndidzayimba nyimbo, inde ndidzayimba nyimbo zotamanda ndi moyo wanga wonse.

2Dzukani, zeze ndi pangwe! Ine ndidzadzutsa mʼbandakucha.

3Ndidzakutamandani Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba za Inu pakati pa anthu a mitundu ina.

4Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kutalika kwake kuposa kumwamba; kukhulupirika kwanu kumafika mlengalenga.

5Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba, ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi.

6Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.

7Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwachipambano Ine ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayesa chigwa cha Sukoti.

8Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu.

9Mowabu ndi mbale yanga yosambiramo ndidzaponya nsapato zanga pa Edomu; ndidzafuwula mopambana pa Filisitiya.”

10Ndani adzandifikitsa ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu?

11Kodi sindinu Mulungu, Inu amene mwatikana ndipo simuperekezanso magulu athu ankhondo?

12Tithandizeni ife kulimbana ndi mdani, pakuti thandizo la munthu ndi lopanda pake.

13Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano, ndipo adzapondereza pansi adani athu.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath