MASALIMO 101
1Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama; kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
2Ndidzatsata njira yolungama; nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzayenda mʼnyumba mwanga ndi mtima wosalakwa.
3Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa pamaso panga. Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro; iwo sadzadziphatika kwa ine.
4Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine; ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.
5Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera.
6Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, kuti akhale pamodzi ndi ine; iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa adzanditumikira.
7Aliyense wochita chinyengo sadzakhala mʼnyumba mwanga. Aliyense woyankhula mwachinyengo sadzayima pamaso panga.
8Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu onse oyipa mʼdziko; ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa mu mzinda wa Yehova.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath