MIYAMBO 10
1Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.
2Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
3Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala; koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.
4Wochita zinthu mwaulesi amasauka, koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.
5Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru, koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.
6Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama, koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.
7Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso, koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.
8Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.
9Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
10Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto, koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.
11Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo, koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.
12Udani umawutsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.
13Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu, koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.
14Anzeru amasunga chidziwitso koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.
15Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.
16Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama, koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.
17Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo, koma wonyoza chidzudzulo amasochera.
18Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.
19Mawu akachuluka zolakwa sizisowa, koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.
20Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.
21Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri; koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.
22Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
23Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa, koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.
24Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira; chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.
25Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa, koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.
26Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso, ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.
27Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo; koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.
28Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe, koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.
29Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino, koma wochita zoyipa adzawonongeka.
30Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.
31Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru, koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula, koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath