Chikhristu
kubwerera

NEHEMIYA 7

1Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa.

2Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena.

3Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”

4Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe.

5Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

6Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.

7Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:

8Zidzukulu za Parosi2,172

9Zidzukulu za Sefatiya372

10Zidzukulu za Ara652

11Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu)2,818

12Zidzukulu za Elamu1,254

13Zidzukulu za Zatu845

14Zidzukulu za Zakai760

15Zidzukulu za Binuyi648

16Zidzukulu za Bebai628

17Zidzukulu za Azigadi2,322

18Zidzukulu za Adonikamu667

19Zidzukulu za Abigivai2,067

20Zidzukulu za Adini655

21Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)98

22Zidzukulu za Hasumu328

23Zidzukulu za Bezayi324

24Zidzukulu za Harifu112

25Zidzukulu za Gibiyoni95.

26Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa188

27Anthu a ku Anatoti128

28Anthu a ku Beti-Azimaveti42

29Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti743

30Anthu a ku Rama ndi Geba621

31Anthu a ku Mikimasi122

32Anthu a ku Beteli ndi Ai123

33Anthu a ku Nebo winayo52

34Ana a Elamu wina1,254

35Zidzukulu za Harimu320

36Zidzukulu za Yeriko345

37Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono721

38Zidzukulu za Senaya3,930.

39Ansembe anali awa: A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa)973

40Zidzukulu za Imeri1,052

41Zidzukulu za Pasi-Huri1,247

42Zidzukulu za Harimu1,017.

43Alevi anali awa: A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya74.

44Anthu oyimba: Zidzukulu za Asafu148.

45Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu zaSalumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai138.

46Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu zaZiha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,

47Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni

48Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,

49Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,

50Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,

51Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,

52Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,

53Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,

54Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,

55Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema

56Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.

57Zidzukulu za antchito a Solomoni: Zidzukulu zaSotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida

58zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,

59zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatiluzidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.

60Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo392.

61Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.

62Zidzukulu zaDelaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda642.

63Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa: zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).

64Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo.

65Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

66Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360.

67Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245.

68Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245.

69Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

70Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530.

71Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250.

72Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

73Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo. Ezara Awerenga Malamulo Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath