Chikhristu
kubwerera

MALAKI 4

1Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi.

2Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.

3Tsiku limenelo inu mudzapondereza anthu oyipa; adzakhala phulusa ku mapazi anu pa tsiku limene Ine ndidzachite zinthu zimenezi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

4Kumbukirani zophunzitsa za mtumiki wanga Mose, malamulo ndi malangizo amene ndinamupatsa pa Horebu kuti awuze Aisraeli onse.

5“Taonani, ndidzakutumizirani mneneri Eliya lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.

6Iye adzabweza mitima ya makolo kwa ana awo, ndi mitima ya ana kwa makolo awo. Kupanda kutero ndidzabwera kudzakantha dziko lanu ndi temberero.”

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath