YOSWA 20
1Pambuyo pake Yehova anati kwa Yoswa:
2“Uza Aisraeli kuti apatule mizinda yopulumukiramo, monga ine ndinakulangizira kudzera mwa Mose,
3kuti aliyense amene wapha munthu mosazindikira osati mwadala azithawirako. Motero adzatetezedwa kwa wolipsira.
4Ngati munthu wathawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, akafike pa malo oweruzira milandu amene ali pa chipata cha mzindawo ndipo akafotokoze mlandu wake pamaso pa akuluakulu a mzindawo. Kenaka iwo adzamulola kulowa mu mzinda wawo ndi kumupatsa malo woti akhale nawo.
5Ngati munthu wolipsirayo amutsatira komweko atsogoleriwo asapereke munthu wakuphayo chifukwa anapha Mwisraeli mnzakeyo mosazindikira, osati mwachiwembu.
6Munthu wakuphayo adzakhalabe mu mzindawo mpaka atayimbidwa mlandu pamaso pa gulu lonse, ndiponso mpaka atamwalira mkulu wa ansembe amene akutumikira pa nthawiyo. Pamenepo munthuyo atha kubwereranso ku mudzi kwawo kumene anachoka mothawa kuja.”
7Choncho iwo anapatula Kedesi mʼdera la Galileya ku mapiri a Nafutali, Sekemu ku mapiri a Efereimu, ndi Kiriati Ariba (ndiye Hebroni) ku mapiri a Yuda.
8Kummawa kwa Yorodani, mʼmapiri a chipululu a kummawa kwa Yeriko, anapatula Bezeri pakati pa dera la fuko la Rubeni. Anapatulanso Ramoti ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi, ndiponso Golani ku Basani mʼdera la fuko la Manase.
9Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraeli onse ngakhalenso mlendo wokhala pakati pawo. Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi ankathawira ku mizinda imeneyi. Munthu wolipsira sankaloledwa kuti aphe munthu wothawayo ngati mlandu wake sunazengedwe pamaso pa gulu lonse.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath