Chikhristu
kubwerera

YOBU 35

1Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti,

2“Kodi mukuganiza kuti mukukhoza? Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’

3Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani, ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’

4“Ine ndikufuna ndikuyankheni inu pamodzi ndi abwenzi anu omwe.

5Yangʼanani kumwamba ndipo muone mitambo imene ili kutali ndi inuyo.

6Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani? Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye?

7Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani? Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu?

8Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo, ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.

9“Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa; akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu.

10Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga, amene amatisangalatsa nthawi ya usiku,

11amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’

12Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa.

13Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake; Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.

14Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti Iye saona zimene zikuchitika. Iye adzaweruza molungama ngati inu mutamudikira

15ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango, zoyipa zambiri zimene anthu amachita,

16abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake, mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.”

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath