YOBU 12
1Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2“Ndithudi inuyo ndinu anthu ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!
3Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu; ineyo sindine munthu wamba kwa inu. Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?
4“Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga, ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha. Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!
5Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka. Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.
6Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere, ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino, amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.
7“Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa, kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;
8kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa, kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.
9Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?
10Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse, ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.
11Kodi khutu sindiye limene limamva mawu monga mmene lilime limalawira chakudya?
12Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba? Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?
13“Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.
14Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso. Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.
15Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma; akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.
16Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana; munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.
17Iye amalanda aphungu nzeru zawo ndipo amapusitsa oweruza.
18Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.
19Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.
20Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.
21Iye amanyoza anthu otchuka ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.
22Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.
23Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso; amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.
24Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi; amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.
25Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira; Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath