Chikhristu
kubwerera

YEREMIYA 24

1Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, anthu aluso ndi akatswiri a ku Yuda ndi kupita nawo ku Babuloni. Pambuyo pake Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu atayikidwa pa khomo pa Nyumba ya Yehova.

2Mʼdengu limodzi munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Mʼdengu linalo munali nkhuyu zoyipa kwambiri zosati nʼkudya.

3Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ndikuona nkhuyu zabwino kwambiri ndi nkhuyu zoyipa zosati nʼkudya.”

4Tsono Yehova anandiwuza kuti,

5“Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Anthu a ku Yuda amene ndinawachotsa ku malo ano nʼkupita nawo ku ukapolo ku dziko la Ababuloni ndikuwafanizira ndi nkhuyu zabwinozi.

6Ndidzaonetsesa kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzabwera nawonso ku dziko lino. Ndidzawamanga osati kuwapasula; ndidzawadzala osati kuwazula.

7Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ndine Yehova. Adzakhala anthu anga ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, chifukwa adzabwerera kwa Ine ndi mtima wawo wonse.

8“ ‘Koma monga nkhuyu zoyipa zija, zomwe ndi zoyipa kwambiri zosati nʼkudya,’ Yehova akuti, ‘ndi mmene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi otsala a mu Yerusalemu, kaya adzakhala ali mʼdziko muno kapena mʼdziko la Igupto.

9Ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa maufumu onse a dziko lapansi, chinthu chonyozeka ndi chopandapake, chinthu chochitidwa chipongwe ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzawabalalitsira.

10Ndidzawatumizira nkhondo, njala ndi mliri mpaka atawonongedwa mʼdziko limene ndinawapatsa iwo ndi makolo awo.’ ”

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath