Chikhristu
kubwerera

YESAYA 46

1Beli wagwada pansi, Nebo wawerama; nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo. Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe. Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.

2Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo; sizikutha kupulumutsa katunduyo, izo zomwe zikupita ku ukapolo.

3Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo, inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli, Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu, ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.

4Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi ndidzakusamalirani ndithu. Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani, ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.

5“Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani? Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?

6Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.

7Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo; amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo. Singathe kusuntha pamalo pakepo. Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha; kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.

8“Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi, Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.

9Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana; chifukwa Ine ndine Mulungu ndipo palibe wina ofanana nane.

10Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.

11Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa. Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa. Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi; zimene ndafuna ndidzazichitadi.

12Ndimvereni, inu anthu owuma mtima, inu amene muli kutali ndi chipulumutso.

13Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa; sichili kutali. Tsikulo layandikira ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath