YESAYA 25
1Yehova ndinu Mulungu wanga; ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu, pakuti mwachita zodabwitsa zimene munakonzekeratu kalekale mokhulupirika kwambiri.
2Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala. Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja, linga la anthu achilendo lero si mzindanso ndipo sidzamangidwanso.
3Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani; mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.
4Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka, mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake. Mwakhala ngati pobisalirapo pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa. Pakuti anthu ankhanza ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,
5ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma. Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo. Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha, inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.
6Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino. Phwando la nyama yonona ndi vinyo wabwino kwambiri.
7Iye adzachotsa kulira kumene kwaphimba anthu ngati nsalu. Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.
8Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya, Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso mwa munthu aliyense; adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi, Yehova wayankhula.
9Tsiku limenelo iwo adzati, “Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu; ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa. Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira; tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”
10Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake; ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo, ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.
11Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo, ngati mmene amachitira munthu wosambira. Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo ngakhale luso la manja awo.
12Iye adzagumula malinga awo ataliatali ndipo adzawagwetsa ndi kuwaponya pansi, pa fumbi penipeni.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath