Chikhristu
kubwerera

HOSEYA 1

1Awa ndi mawu amene Yehova anayankhula kwa Hoseya mwana wa Beeri pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda ndiponso pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Yowasi mfumu ya ku Israeli.

2Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.”

3Motero Hoseya anakwatira Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu, ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna.

4Tsono Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti Yezireeli, pakuti ndili pafupi kulanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene anawapha ku Yezireeli ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israeli.

5Tsiku limenelo ndidzathyola uta wa Israeli mʼchigwa cha Yezireeli.”

6Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse.

7Komatu ndidzaonetsa chikondi pa nyumba ya Yuda; ndipo ndidzawapulumutsa, osati ndi uta, lupanga kapena nkhondo, kapena akavalo ndi okwerapo ake, koma ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.”

8Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri anabereka mwana wina wamwamuna.

9Pamenepo Yehova anati, “Umutche dzina loti Sianthuanga,” pakuti inu si ndinu anthu anga ndipo Ine si ndine Mulungu wanu.

10“Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’

11Anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Israeli adzasonkhananso pamodzi ndipo adzasankha mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka mʼdzikomo, pakuti tsiku la Yezireeli lidzakhala lalikulu kwambiri.”

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath