HOSEYA 12
1Efereimu amadya mpweya; tsiku lonse amasaka mphepo ya kummawa ndipo amachulukitsa mabodza ndi chiwawa. Amachita mgwirizano ndi Asiriya ndipo amatumiza mphatso za mafuta a olivi ku Igupto.
2Yehova akuyimba mlandu Yuda; Iye adzalanga Yakobo molingana ndi makhalidwe ake, adzamulanga molingana ndi ntchito zake.
3Akali mʼmimba mwa amayi ake, Yakobo anagwira chidendene cha mʼbale wake; iye atakula analimbana ndi Mulungu.
4Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana; analira napempha kuti amukomere mtima. Mulungu anakumana naye ku Beteli ndipo anayankhula naye kumeneko,
5Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Yehova ndiye dzina lake lotchuka!
6Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu; pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama, ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.
7Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo; iyeyo amakonda kubera anthu.
8Efereimu amadzitama ponena kuti, “Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri. Palibe amene angandiloze chala chifukwa cha kulemera kwanga.”
9“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa mu Igupto. Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti, monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.
10Ndinayankhula ndi aneneri, ndinawaonetsa masomphenya ambiri, ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”
11Kodi Giliyadi ndi woyipa? Anthu ake ndi achabechabe! Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala? Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala mʼmunda molimidwa.
12Yakobo anathawira ku dziko la Aramu, Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi, ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.
13Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto; kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.
14Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri. Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa. Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath