Chikhristu
kubwerera

HOSEYA 11

1“Israeli ali mwana, ndinamukonda, ndipo ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.

2Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana iwo amandithawa kupita kutali. Ankapereka nsembe kwa Abaala ndipo ankafukiza lubani kwa mafano.

3Ndi Ine amene ndinaphunzitsa Efereimu kuyenda, ndipo ndinawagwira pa mkono; koma iwo sanazindikire kuti ndine amene ndinawachiritsa.

4Ndinawatsogolera ndi zingwe zachifundo cha anthu ndi zomangira za chikondi; ndinachotsa goli mʼkhosi mwawo ndipo ndinawerama nʼkuwadyetsa.

5“Sadzabwerera ku Igupto, koma Asiriya ndiye adzakhala mfumu yawo pakuti akana kutembenuka.

6Malupanga adzangʼanima mʼmizinda yawo, ndipo adzawononga mipiringidzo ya zipata zawo nadzathetseratu malingaliro awo.

7Anthu anga atsimikiza zondifulatira Ine. Ngakhale atayitana Wammwambamwamba, sizidzatheka kuti Iye awakwezenso.

8“Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu? Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli? Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima? Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero; chifundo changa chonse chikusefukira.

9Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa, kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu. Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu, Woyerayo pakati panu. Sindidzabwera mwaukali.

10Iwo adzatsatira Yehova; Iye adzabangula ngati mkango. Akadzabangula, ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.

11Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Igupto, ngati nkhunda kuchokera ku Asiriya. Ine ndidzawakhazikanso mʼnyumba zawo,” akutero Yehova.

12Efereimu wandizungulira ndi mabodza, nyumba ya Israeli yandizungulira ndi chinyengo. Ndipo Yuda wawukira Mulungu, wawukira ngakhale Woyerayo amene ndi wokhulupirika.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath