EZARA 2
1Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake.
2Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana). Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:
3Zidzukulu za Parosi2,172
4zidzukulu za Sefatiya372
5zidzukulu za Ara775
6zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu)2,812
7zidzukulu za Elamu1,254
8zidzukulu za Zatu945
9zidzukulu za Zakai760
10zidzukulu za Bani642
11zidzukulu za Bebai623
12zidzukulu za Azigadi1,222
13zidzukulu za Adonikamu666
14zidzukulu za Bigivai2,056
15zidzukulu za Adini454
16zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)98
17zidzukulu za Bezayi323
18zidzukulu za Yora112
19zidzukulu za Hasumu223
20zidzukulu za Gibari95.
21Anthu a ku Betelehemu123
22Anthu aamuna a ku Netofa56
23Anthu aamuna a ku Anatoti128
24Anthu aamuna a ku Azimaveti42
25Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti743
26Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba621
27Anthu aamuna a ku Mikimasi122
28Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai223
29Anthu aamuna a ku Nebo52
30Anthu aamuna a ku Magaibisi156
31Anthu aamuna a ku Elamu wina1,254
32Anthu aamuna a ku Harimu320
33Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono725
34Anthu aamuna a ku Yeriko345
35Anthu aamuna a ku Sena3,630.
36Ansembe anali awa: Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa)973
37Zidzukulu za Imeri1,052
38Zidzukulu za Pasuri1,247
39Zidzukulu za Harimu1,017.
40Alevi anali awa: Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya)74.
41Anthu oyimba nyimbo anali awa: Zidzukulu za Asafu128.
42Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai139.
43Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Zidzukulu zaZiha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
44zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,
45zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,
46zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,
47zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,
48zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,
49zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,
50zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,
51zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
52zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
53zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,
54zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.
55Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi: Zidzukulu zaSotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda,
56zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
57zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu,zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami.
58Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali392.
59Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
60Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali652.
61Ndi ena pakati pa ansembe anali awa: Zidzukulu zaHobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)
62Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo.
63Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.
64Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360,
65kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200.
66Anali ndi akavalo 736, nyulu 245,
67ngamira 435 ndi abulu 6,720.
68Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale.
69Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.
70Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath