EZEKIELI 35
1Yehova anandiyankhula kuti:
2“Iwe mwana wa munthu, yangʼana phiri la Seiri; yankhula moliyimba mlandu ndipo
3awawuze anthu a kumeneko kuti zimene ndikuyankhula Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu anthu a ku mapiri a Seiri ndikudana nanu. Ndidzatambasula dzanja langa kulimbana nanu, ndipo ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu.
4Mizinda yanu ndidzayisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzasanduka chipululu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5“Munali adani a Israeli nthawi zonse, ndipo munkalola kuti Aisraeli aphedwe pa nkhondo pa nthawi ya mavuto awo, pa nthawi imene chilango chawo chinafika pachimake.
6Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzakukanthani. Imfa idzakulondolani. Popeza sunadane nako kukhetsa magazi, imfa idzakulondola.
7Phiri la Seiri ndidzalisandutsa chipululu ndipo ndidzapha onse amene amapita nabwerera kumeneko.
8Ndidzaza mapiri ake ndi mitembo. Ophedwa pa nkhondo adzagwera pa zitunda zanu, zigwa zanu ndi mʼmitsinje yanu yonse.
9Ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu mpaka muyaya, ndipo mʼmizinda yanu simudzakhalanso anthu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
10“Inu munanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu, Yuda ndi Israeli, pamodzi ndi mayiko awo omwe idzakhala yathu.’ Munanena chomwechi ngakhale kuti Ine Yehova ndinali momwemo.
11Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzachita nanu monga munachita ndi anthu a ku Yuda ndi Israeli poonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu pa iwo. Ndikadzakulangani mudzandidziwadi pakati panupo.
12Ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndinamva mawu anu onse onyoza amene munanena molimbana ndi mapiri a Israeli. Inu munati, ‘Mapiri a Israeli asanduka bwinja, ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwawononge.’
13Mawu anu amene munayankhula monyada kundinyoza Ine ndinawamva.
14Ine Ambuye Yehova ndikuti: Dziko lonse lapansi lidzasangalala pamene ndidzakusandutsani bwinja.
15Monga momwe inu munasangalala pamene anthu anga Aisraeli anagwa, Inenso ndidzakuchitani chimodzimodzi. Udzasanduka bwinja, iwe Phiri la Seiri, iwe ndi dziko lonse la Edomu. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath