EZEKIELI 19
1“Imba nyimbo ya madandawulo, kuyimbira akalonga a ku Israeli.
2Uzinena kuti, “ ‘Amayi ako anali ndani? Anali ngati mkango waukazi! Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna; unkalera ana ake pakati pa misona.
3Unalera mmodzi mwa ana ake, ndipo mwanayo anasanduka mkango wamphamvu. Unaphunzira kugwira nyama, ndipo unayamba kudya anthu.
4Anthu amitundu anamva za mkangowo, ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo. Iwo anawukoka ndi ngowe kupita nawo ku dziko la Igupto.
5“ ‘Amayi aja ataona kuti mwana ankamukhulupirira uja wagwidwa ndi kuti chiyembekezo chake chapita padera, amayiwo anatenganso mwana wina namusandutsa mkango wamphamvu.
6Unkayendayenda pakati pa mikango inzake, pakuti tsopano unali mkango wamphamvu. Unaphunzira kugwira nyama ndipo unayamba kudya anthu.
7Unagwetsa malinga awo, ndikuwononga mizinda yawo. Onse a mʼdzikomo anachita mantha chifukwa cha kubangula kwake.
8Pamenepo mitundu ya anthu, makamaka ochokera madera ozungulira, inabwera kudzalimbana nawo. Anawutchera ukonde wawo, ndipo tsiku lina unagwera mʼmbuna mwawo.
9Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga. Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ndipo mfumuyo inawuponya mʼndende ndi cholinga choti liwu lake lisamamvekenso ku mapiri a Israeli.
10“ ‘Amayi ako anali ngati mpesa mʼmunda wamphesa wodzalidwa mʼmbali mwa madzi. Unabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri chifukwa cha kuchuluka kwa madzi.
11Nthambi zake zinali zolimba, zoyenera kupangira ndodo yaufumu. Unatalika nusomphoka pakati pa zomera zina. Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake, ndi nthambi zake zambiri.
12Koma unazulidwa mwaukali ndipo unagwetsedwa pansi. Unawuma ndi mphepo ya kummawa, zipatso zake zinayoyoka; nthambi zake zolimba zinafota ndipo moto unapsereza mtengo wonse.
13Ndipo tsopano anawuwokeranso ku chipululu, dziko lowuma ndi lopanda madzi.
14Moto unatulukanso mu mtengomo ndi kupsereza nthambi ndi zipatso zake. Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowo yoyenera kupangira ndodo yaufumu. Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’ ”
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath