AMOSI 7
1Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene.
2Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
3Kotero Yehova anakhululuka. Yehovayo anati, “Izi sizidzachitika.”
4Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko.
5Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
6Kotero Yehova anakhululuka. Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.”
7Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma.
8Ndipo Ambuye anandifunsa kuti, “Amosi, nʼchiyani ukuonachi?” Ine ndinayankha kuti, “Chingwe chowongolera khoma.” Ndipo Yehova anati, “Taona, Ine ndikuyika chingwe chowongolerachi pakati pa anthu anga, Aisraeli; sindidzawalekereranso.
9“Malo achipembedzo a Isake adzawonongedwa ndipo malo opatulika a Israeli adzasanduka bwinja; ndidzagwetsa nyumba ya Yeroboamu ndi lupanga langa.”
10Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo.
11Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi: “ ‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga, ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’ ”
12Ndipo Amaziya anawuza Amosi kuti, “Choka, mlosi iwe! Bwerera ku dziko la Yuda. Uzikalosera kumeneko ndipo anthu a kumeneko azikakudyetsa.
13Usanenerenso ku Beteli, chifukwa kumeneko ndi malo opatulika a mfumu ndiponso ndi malo a nyumba yachipembedzo yaufumu.”
14Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu.
15Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’
16Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti, “ ‘Usanenere zotsutsa Israeli, ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ”
17“Tsono zimene akunena Yehova ndi izi: “ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu, ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa, ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu. Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’ ”
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath