Chikhristu
kubwerera

2 MBIRI 27

1Yotamu anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. Dzina la amayi ake linali Yerusa mwana wa Zadoki.

2Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga anachitira Uziya abambo ake, kupatula kuti iyeyo sanalowe mʼNyumba ya Yehova. Komabe anthu anapitirira kuchita zoyipa.

3Yotamu anamanganso chipata chakumtunda cha Nyumba ya Yehova ndipo anagwira ntchito yayikulu yomanga khoma la ku phiri la Ofeli.

4Iye anamanga mizinda mʼmapiri a ku Yuda ndipo anamanganso malinga ndi nsanja mʼmadera a ku nkhalango.

5Yotamu anachita nkhondo ndi mfumu ya Aamoni ndipo anawagonjetsa. Chaka chimenecho Aamoni anapereka makilogalamu 3,400, matani 1,000 a tirigu ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni anabweretsa zinthu zomwezi chaka chachiwiri ndi chachitatu.

6Yotamu anakula mphamvu chifukwa anayenda molungama pamaso pa Yehova Mulungu wake.

7Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Yotamu, kuphatikizapo nkhondo zake zonse ndi zinthu zina zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda.

8Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16.

9Yotamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. Ndipo Ahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath