Chikhristu
kubwerera

1 TIMOTEYO 2

1Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika.

2Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.

3Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu,

4amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi.

5Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.

6Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera.

7Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.

8Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.

9Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.

10Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.

11Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu.

12Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete.

13Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava.

14Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa.

15Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath